Za Daniel Phiri Ndikumva Ndiiwe Mwina Unampatsa Ndiiwe Poti Ndiwe Pilirani Phiri…
Pilirani Phiri; “potsatira kutuluka kwa lipoti la imfa ya Bingu pali chyembekezo kuti inu a Kaliati muntha kumangidwa, muli ndi mantha??
Patricia Kaliati; “Ha, ha, ha, pilirani ine Patricia Kaliati mwana wa botomani ndilibe mantha.”
Pilirani Phiri; “komatu lipoti likusonyeza kuti mumafuna kulanda boma?”
Patricia Kaliati; ” Timafuna kulanda boma lake liti, popeza nthawi imeneyo panalibe amene analumbiritsidw a kuti akhale mtsogoleri koma inu muziopa mulungu.”
Pilirani Phiri; “Lipoti likunenanso kuti mamafuna kuti Peter wa mutharika kuti atenge mpando wautsogoleri wa dziko lino”
Patricia Kaliati; “ndichifukwa chake mulungu akukulangani, chimanga thumba limodzi K10,000 Simunati Mulungu azikulanganibe. ”
Pilirani Phiri; “zinakhala bwanji kuti Bingu akhale Daniel Phiri pamene amapita naye kuchipatala ku South Africa, munabalalika kwambiri eti?”
Patricia Kaliati; “za Daniel Phiri ndikumva ndiiwe mwina unampatsa ndiiwe poti ndiwe pilirani Phiri.
No comments! Be the first commenter?