Anthu olusa oshala ku Mbayani mu mzinda wa Blantyre aphwanya manyumba 13 a sten ina yemwe akumuganizira kuti inaduwitsa nfana wa mkulu wake kamba kolimbirana ma ndalama a nyumba za lent.

Nkhaniyi ikuti Malemu Lusungu yemwe mai ake anamusiyira nyumba ataduwa ma ages avayawa, amakhilashana ndi Aunt akewo omwe dinyero za lent amangophaka okha.

Zitafika povuta ndipamene Aunt a Lusungu ana hire ma pauda kuti aphike mfana wa Chemwali awo omwe anasiya maden amalimbirana ndi nfanayo. Ndiye anyamata aganyu anapamantha mwana, kumuphiriphitha, kumugagada mpaka nfana kudu… kuduwa.

Omwe atithathitsa nkhaniyi ati atamuduwitsa nfana wamugetoyu anatenga body lake ndikuika mukhitchini, mkugula ka botolo kamowa (stout) mkushalitsa pambalipa mkudzamutentha face kuti aziti wafa ndingozi malinga chamayakidwe.

Ndiye chinatsitsa dzaye ndichoti ma neba anathaima za nkhani ndikuika ma question mark mpaka kuwapanikiza ma dolo a ganyu omwe anawulura.

Ma bwana amu gheto aku Mbayani setha nkhaniyi anakwiya heavy ndkuvaya ku den kwa niste kuja ndikuyamba violence man. Ndiye kunali kudoda aliyense anali pafupi, kuphwanya mawindo ndi ngini zambiri.

Komanso faz inathatha ma plasma, ma cooker, ma fridge. kudzapeza kuti mboba imodzi yaseza cooker pali mapoto nsima ikubwata osaiphula tindiwo pompo pokafika kuden ngini zapsa.

Maliro anfana watisiya ayikidwa mawa panopa thupi lili ku ma ice ku mortuary. Nkhani yovetsa chisoni kwambiri kuti faz ikumapondelezabe ana amasiye.