Pamene mphekesela yakula yoti msogoleli wa dziko lino Professor Peter Mutharika sakupeza bwino ndipo wagonekedwa mchipatala china ku United States of America, Nyumba ya boma yalengeza kuti Mutharika abwelela kumudzi la mulungu.

Izi zawika kuchokela mu uthenga omwe wasindikizidwa pasamba la Nyumba yofalitsa nkhani boma mdziko muno la Malawi Broadcasting Corporation (MBC 1).

Malingana ndi nyumbayi, uthenga wakubwela kwa a Mutharika wachokela kwa ofalisa nkhani ku nyumba ya chifumu yemwe ali ndi msogoleliyu ku New york, Mgeme Kalirani.

Kalirani wauza nyumbayi kuti Mutharika akuyembekezeleka kuzafika pa Kamuzu International Airport(KIA) ku Lilongwe 1 koloko masana.

Mukafuna kuziwa zambiri pa ulendowu pitilizani kuwelenga nkhani zathu

Subscribe to our Youtube Channel: