Ndi zinthu zomvetsa chisoni komaso zokhuza ku mtundu onse wa Malawi poganizira kuti vuto la kuzimazima kwa magetsi silikusintha ngakhale pamene talowa mwezi omwe akhistu amakhala akukondwelera kubadwa kwa mpulumutsi wawo ndipo zochitika zambiri m`mweziwu zimafuna magetsi.

Ndi mwa chikhalidwe cha akhristu pa dziko lonse lapansi kuti mwezi wa December umadzadza ndi zikondwelero zosiyanasiyana pokumbukira kubadwa kwa mpulumutsi yesu khristu kotero zina mwa izo sizingalongosoke ngati palibe mphamvu ya magetsi.

an illustrative picture

Tangoganizani, muli mkati mwa chisangalaro koma mosayembekezeka, a ESCOM mkuzadulaso mphamvu za magetsi, mungamve bwanji kumtima kwanu?

Chabwino ambiri mwa inu simukufuna olo mpang`ono pomwe mutaganizira za izi chifukwa chingakhale chinthu chopweteka zitakuchitikirani inu pomwe mulibeso podalira inde ngakhale ma jenereta akutionongera mtendere wa m`makutu athu tikamadutsa mtawuniwa.

Koma dziwaniso kuti izi zili ndi kuthekera konse kozachitika maka pa tsiku la chikondweleloro poti pano M`Malawi aliyense wasanduka m`neneri kotero tikumatha kulosera za kuthima kwa magetsi komwe kungathe kuzachitika masiku ali mkudza.

Koma mwina mwa chisomo cha mulungu mwadutsa opanda matsoka alionse ochokera ku escom pa tsikulo, koma tsoka mkuzadza pa tsiku lokondwelera kulowa mchaka cha tsopano, tangoganizani?

Mwachidziwikire ambiri mwa inu mungakhale opanda chiyembekezo ndi chaka chatsopano chomwe malo mochilowa mwa mtendere mwachilowa muli mumdima.

Mwachidule izi zingangotanthauza kuti tikuyembekezera kukumana ndi mavuto ena oposa omwe tatopa nawo kale mu chaka chimenechi zomwe zili ngati kumuuza munthu yemwe akupsa ndi moto wa ku gahena kuti ayembekezereso chilango china chomwe chili mkudza mwa iye.

Tikakukumbuka bwino lomwe, tate wathu wa dziko lino olemekezeka Arthur Peter Muntharika adalonjeza mtundu wa Malawi kuti vuto la kuzimazima kwa magetsi litha m`mwezi umenewu wa December kotero amalawi ambiri ali tcheru kuti awone izi zikuchitika poti pakadali pano mweziwu siunathe.

Ngakhale izi zili choncho, bungwe lomwe likuthandizana ndi Escom pa nkhani ya mphamvu ya magesti (Egenco) lidalengezaso nalo kuti vuto lakuzimazima kwa magetsili likuyembekezeka kutha chaka cha mawa mwezi wa march zomwe zili zosemphana ndi zomwe mtsogoleri wa dziko lino adalonjeza mtundu wake.

Koma pakadali pano, amalawi akuyembekezabe kuti aone kuwala kwa magetsi kuti Khirimisi yawo ikhale yopambana.