Anthu olusa pa msika wa kabwazi m`boma la Dedza aboola khoma la nyumba ya polisi ndikupha munthu yemwe anatsekeredwa kamba koganiziridwa uchifwamba.

anthu aboola khoma la nyumba ya polisi

Malingana ndi M`neneri wa polisi ku Dedza a Edward Kabango, nkhaniyi yachitika lachitatu pa 24 januware.

Ma lipoti a nkhaniyi akuti, munthuyo anapanga hayara njinga ya moto kuti akamusiye ku Kafere komweso kuli nkhalango ya Dzalanyama.

“Ali mkati mwa ulendowo, mwini njingayo anadabwa ndi munthuyo poti samafotokoza bwino lomwe komwe amapita.

“Kotero, mwini njingayo adanamiza mbavayo kuti njinga yake yatha mafuta oyendera ndipo pa chifukwachi ulendowo supitilira, atero a Kabango.

Izi zili chomwechi, mwini njingayo anapeza njira yodziwitsa anthu ena omwe anabwera kudzagwira mbavayo ndikuipititsa pa polisi ya Kabwazi komwe inatsekeredwa.

Koma athu a m`mudzi atamva izi anathamangira ku polisi konko kukaumiliza apolisi kuti atulutse munthuyo ndi cholinga choti alange okha.

Apolisi atakana kumvera anthuwo, chipolowe chinabuka ndipo anthuwo anaboola khoma la nyumba la polisiyo ndikumutulutsa, komaso kupha munthuyo.

Ma lipoti akuti, mderali muli mbava zonga izi zomwe zimanamizira kutenga hayara ya njinga ndi cholinga chokapha mwini njingayo komaso kumubera njinga yakeyo ndi ndalama.