Mzibambo wina mu dziko la South Korea wadabwitsa anthu atapha galu wa neba wake, mkumuphika kenako mkumuitanira mwiniwake galuyo ku nkhomaliro.
Malingana ndi nyumba zolemba nkhani mu dzikolo, Mzibamboyo yemwe akuti ndi wazaka 61 anapha galuyo ndi mwala kamba koti amapanga phokoso akamakuwa.
“atakomoka chifukwa cha ululu wodza kamba kogendedwako, Mzibamboyo anafinya galuyo pakhosi kenako mkumutengera m’nyumba mwake komwe anakamupanga ndiwo”, apolosi mdera la Pyeongtaek anauza atolankhani.
Iye akuti sanasiire pompo koma kuitana mwini galuyo kuti azadye nawo ndiwoyo.
Nkhaniyi inadziwika pomwe anthu ena ozungulira atatsina khutu mwini galuyo pamene anadandaula za kusowa kwa galu wake patatha masiku angapo.
Nyama ya galu yakhala ikutengedwa ngati ndiwo mu dziko la South Korea kwa nthawi yaitali ndithu. Koma malingana ndi kusintha kwa zinthu, anthu mdzikomo anayamba kunyadira agalu ndi kumaatenga ngati ziweto osati ndiwo moti nkhaniyi yadabwitsa anthu ena achichepere omwe angobadwa zaka zatsopano mu dzikolo.