Mzungu wina anatsala pang’ono kuonetsedwa zakuda atatchula munthu wakuda kuti ndi kapolo pa tsamba lina la mchezo la pa facebook.
Nkhaniyi ikuti Mike Harper ndi m’modzi mwa anthu ongobwera mdziko muno omwe ali mgulu la pa facebook lotchedwa “Lilongwe Expat Leaving/Arriving momwe amadziwitsana wina akamapita, kubwera komaso komwe angapeze zinthu zoyenelera muno M’malawi.
Pa tsikuli, mzungu wina otchedwa Pennie Ginn amabwelera dziko la kwawo choncho analemba pa tsambali kuti akubwelera koma zachisoni ndi zoti akusiyana ndi munthu wokuda yemwe amamuthandiza kugwira ntchito za pakhomo kunyumba kwake makaso kuyang’anira ana ake.
Ndemanga ya a Ginn pa za watchito wawo inali yodziwitsa azungu anzake pa gululi kuti ngati angafune munthu owagwilira ntchito okhulupilika atha kutenga yemwe anali owagwilira nchito kunyumba kwawoyo.
Koma Mike Harper anayankha mopanda umunthu ponena kuti, “Iwe, osangomutenga kapolo wakoyo bwanji? Maganizo anga”
Yankholi linadzetsa nkwiyo kwa anthu ena akuda omwe aliso pa gulupuyi omwe nkuona kwawo, amati mzunguyu sadalankhule bwino.
Munthu wina anati, “Ndikukhulipilira ndi otetezedwa konse mkona akuyankhula zopusa ngati izi. Ofunika alongedze ndipo adzipita. Ngati ali ndi umunthu chomwe angachite ndikupepesa basi.”
Mwadzidzi mzunguyu anaganiza zopepesa komabe izi sizinanunkhe kanthu kwa anthu ena omwe anaona zomwe Mr Harper analemba.
Pakadali pano, palibe lipoti lomwe laonetsa chomwe chaachitikira a Harper potsatila ndi kufufuta ndemanga yawo yomwe inautsa nkwiyo wa anthu pa gululi.
No comments! Be the first commenter?