Phungu wa chipani cholamula cha DPP, kuzambwe kwa boma la Ntcheu, Reverend Mwai Kamuyambeni wati chipani chotsutsa cha Malawi Congress mwadzadza njoka zokha zokha zomwe zili ndi milandu yomwe zikuyenera kuyankha kwa a Malawi.

khwimbi la anthu ku msonkhano wa MCP

“Anthu awa akunamiza mtundu wa amalawi ngati ndi oyera mtima komaso olungama koma chonsecho ali ndi milandu yoopsa yomwe akuyenera ayankhe ku mtundu wa a Malawi,” watero kamuyambeni.

Malingana ndi a Kamuyambeni, mamembala ena a chipani cha MCP ali ndi milandu yokupha yomwe mpaka pano sadayankhebe.

Iwo adati sanapatsidwe mwayi owona bambo awo omwe anamwalira zaka zambuyo zapitazo, zomwe zidali kamba ka utsogoleri wa nkhaza wa MCP.

Poyankhulapo za United Transformation Movement (UTM) yomwe mtsogoleri wake ndi olemekezeka a Dr Saulos Chilima, a Kamuyambeni ati atsogoleri a UTM ndi anthu ogawukira komaso owukira.

“Anthu awa ndi njoka. Chipani cha DPP chimasungira dzila la njoka,” atero a Kamuyambeni.

Masiku adzanawo, mtsogoleri wa chipani cha MCP opuma, malemu Hastings Kamuzu Banda komaso mtsogoleri wa pano wa chipanichi, a Dr Lazarus Chakwera adapepesa kamba ka nkhaza zina zomwe anthu ena achipani cha MCP adachitira amalawi.

Mawu a Kamuyambeni akudza  masiku ochepa mtsogoleri wa UTM, a Chilima atayankhula pa msonkhano omwe adachititsa ku Masintha ku Lilongwe kuti akazasankhidwa kukhala mtsogoleri wa dziko lino azayamba kaye wathana ndi anthu omwe ali ndi milandu ya katangale ndipo akubisala mu chipani cholamula cha DPP.