Akuluakulu amabungwe omwe siaboma atsindika kuti zokambirana zawo zikupitilira ndi aphungu a nyumba ya malamulo pa ndondondomeko yofuna kuchotsa pa udindo mtsogoleri wa dziko lino Peter Muthalika mokakamiza kamba koganiziridwa kuti akukhudzidwa ndi katangale.

Kampani ya Pioneer Investments inapatsidwa ntchito yoti ipereke zakudya monga nyama ya mchitini ku polisi ndipo inayika ku buku la ku banki yachipani cha DPP ndalama zokwana K145 Million yomwe yemwe amasayinira ndi Peter Mutharika.

Kamba ka nkhaniyi akuluakulu amabungwewa akhala akuwumiliza Mutharika kuti atule pansi udindo wake ndipo kuti akapanda kutero amuchotsa mokakamiza.

Koma Mutharika wanenetsa kuti sangatule pansi udindo wake kamba kankhaniyi.