Apolisi aku Mozambique anjata asodzi aku Malawi kamba kowedza msomba m’nyanja ya Malawi ku gawo la Mozambique.
Asodzi pafupifupi makumi asanu ndi limodzi akumalawi ananjatidwa sabata latha ndipo malipoti akuonetsa kuti asodziwa anamasulidwa patapita masiku angapo potengere adindo aku Malawi atafufuza zankhaniyi.
Koma maboti pafupifupi asanu ndi awiri sanabwezedwe ndi a polisi aku Mozambique.
Apolisi aku Mozambique anena kuti abweza ma botiwo pokhapokha asodiziwo apeleke k5 million kamba powedza Nsomba popanda chilorezo ku gawo la Mozambique Mu nyanja ya Malawi.
Nyanja a Malawi ili mozunguliridwa ndi maiko a Mozambique ndi Tanzania ndipo nyanjayi maikowa anatengapo gawo pang’ono. Gawo laliku la nyanjali lidatengedwa ndi dziko la Malawi.