Mkulu wina yemwe adali paulendo wopita ku Tanzania kuchokera Ku Lilongwe dzulo wachimina atamwa chakumwa chaukali kwambiri.

Mkuluyi anakwera Ndege ku Lilongwe ndipo iyi adaganiza zokumwa Mowo wa maspirit kuti ulendo asauone kutalika. Mphuno salota kuluyi anamwa Jang’ala mopyoola muyezo.

Ndege itanyamuka ulendo wopita Ku Chileka Airport, mkuluyi adadzichitila chimbudzi muthalauza lake kamba ka Mowawo ndipo mkuluyi amamveka fungo la dzaoneni.

Izi zidapangitsa tiziphadzuwa toyang’anila mundenge kutsitsa m’kuluyi ndege itafika Ku Chileka Airport.