
Apolisi akusunga m’chitokosi driver wina kamba kogunda ndikupha mwana wa zaka zisanu
Published on September 26, 2018 at 11:14 AM by Face of Malawi
Apolisi akusunga m’chitokosi driver wa galimoto lalikulu lonyamula katundu, George Chauluka kamba kogunda ndikupha mwana wa zaka zisanu mu m’zinda wa Lilongwe.
Pa 24 September chaka chino, Chauluka amayendetsa galimoto la m’tundu wa Freight-liner ya kampani ya Chibuku Products Limited ndipo anagunda mwanayo pa nthawi yomwe amabwelera ku ntchito.
Malingana ndi m’neneri wa polisi ya Lingadzi Gift Chitowe, Chauluka anachoka ku kampani yake ya Chibuku yomwe ili ku Kanengo atanyamula zinyasi kupita kwa Kauma komwe amakataya zinthuzi ndipo mwangozi anagunda mwana yemwe amafuna kudutsa pakati pa mateyala a galimotoli.
Chitowe anawonjezera kuti mwanayu amatsanzira anzake omwe amapanga zomwezo koma sanavulale.