Anyamata Asanu Akabaza anjatidwa kamba kosalipira Msonkho

Anyamata Asanu Akabaza anjatidwa kamba kosalipira Msonkho

Published on October 19, 2018 at 10:13 AM by Face of Malawi

84 words • approx. 1 min read

Anyamata akabaza omwe amachita ziwonesero kamba kosakondwa ndi zoti azilipila sonkho pamwezi awanjata m’boma la Salima.

Anyamata okwana 5 awamanga Ku Salima kamba kosalipila ndalama ya sonkho womwe amadula pamwezi kamba kopanga bisinesi ya kabaza

Anyamata anjinga zakabazawa mwezi uliwose amapeleka K3500 Ku Boma ndicholinga Boma lizigwirisa ndalamayi pa nkhani zachitukuko.

Akabaza anadandaula kuti ndikovuta kupanga K3500 yongowapasa a boma popeza iwo kupeza Chakudya kuzera mukabaza akumachita kuchivutikila.

Pakadali pano Boma lawalanda njinga akabaza osakwanisa kulipila sonkho m’bomali.

Zambiri za nkhaniyi tikupatsirani ka nthawi kena.

Subscribe to our Youtube Channel: