Wachiwiri kaotsatira Mtsogoleri wa Chipani cha Malawi Congress (MCP), Harry Mkandawire waombola mzimayi yemwe anapangidwa chitaka ku Rumphi pomupatsa ndalama komaso kumugulira thumba la feteleza.

Malingana ndi mapikitchala komaso ma lipoti omwe anapezeka pa tsamba la intaneti la fecebook, Mzimayiyu anali ndi ndalama zokwana K18,000 zomwe anapita nazo ku msika wina ku Rumphi kuti akagule feteleza.

Koma asanagule feteleza, mayiwa anayamba wagula zakudya zina ndi zina pamsika wa Salaula.

Chodabwitsa chinali chakuti, atafika pogula feteleza anadabwa poona kuti ndalama zomwe anasunga pa chitenje panalibe, malo mwake panapezeka mapepala amkaka wotsegulidwa kale.

Pakumva za nkhaniyi, a Harry Mkandawire anagwidwa ndi chisoni moti anapempha anthu amene angawadziwe mayiwa ndi cholinga chakuti awathandize powapatsa ndalama zomwe amafuna agulire fetelezazo.

“Asakane mayiwa. Ndipanga zotheka kuti ndiapatse K18,000 yomwe amafuna kugulira fetelezayo. Sindimakondwa ndikamaona azimayi akulira. Ndikhala ndili konko kumapeto kwa sabatayi, “ anatero a Mkandawire.

Cha ku m’mawaku, a Mkandawire anatuma anthu kuti akapereke thumba la feteleza komaso ndalama kwa mayiwa monga mwa lonjezo lawo.