
“Ntchito Yofalitsa za Matenda a Shuga ikubwerela M’mbuyo” – Diabetes association of Malawi
Published on November 14, 2018 at 4:12 PM by Face of Malawi
Bungwe la anthu omwe amadwala matenda a Shuga lati kuchepa kwa zipangizo zofalitsira mauthenga a nthendayi m’madera akumidzi ndi chimodzi mwa zinthu zomwe zikubwenzeretsa mmbuyo ntchito yolimbana ndi nthendayi.
Mtsogoleri wa Bungweli, a Clement Mandala anena izi pomwe dziko la Malawi pamodzi ndi mayiko onse padziko lapansi akukumbukira tsiku loganizira za matenda a Shuga pa 14 November chaka chilichonse.
A Mandala anati ndizomvetsa chisoni kuti anthu ambiri akudwala komanso kumwalira ndi matendawa kaamba kosowa upangiri wa momwe angapewere nthendayi.
Source : Yoneco Fm