Bwalo la milandu la Makande ku Chikwawa lalamula bambo Mexon Chaleka azaka 48 kuti akakhale kundende zaka ziwiri ndi miyezi isanu ndi umodzi (6) kaamba koba ng’ombe ziwiri.

Chaleka anapalamula mulanduwu usiku wapa 31 October, 2018 m’mudzi wa Gonyo kwa Ngabu. Usikuwo, Chaleka anali ndi anzake ena awiri ndipo adafika pa khola la Mayi Lucy Kanthema.

“Panthawiyo, Maiwa adali akugona mkhonde la nyumba yawo, ndipo anaona anthu ena atatu akulunjika kukhola lawo.

Atalondola anthu okayikitsawo, mwini khola uja anapeza kuti kholalo ndi losegula ndipo ng’ombe ziwiri mulibe.

Kenako adaona anthu okuba aja chapafupi ndipo adakuwa, zomwe zidapangisa mbava zija kuthawa.

Koma anthu am’mudzimo anazuka mwachangu ndikugwira a Mexon Chaleka.” Constable Foster Benjamin adatero polankhula ndi atolankhani.

Apa, a Chaleka anawalondolera anthu aja komwe anabisa zifuyo zija.

Chaleka anatengeredwa ku polisi ya Ngabu komwe anamusegulira mulandu okuba ng’ombe.

Koma mulandu andaukana pa khoti, ndipo a boma kudzera kwa Constable Mwanyala Goche adabweresa mboni zinayi.

Abomawa anapempha bwalo kuti lipereke chilango chokhwima kwa ozengedwa mulanduwo maka poganiza ndi kabwerebwere ku ndende.

Mu chaka cha 2015, Chaleka anapasidwanso chilango ngati chomwecho pa mulandu okuba mbuzi.

Ndipo popereka chigamulo, oweruza milandu kubwaloli, a Chiyembekezo Phiri anagwirizana ndi maganizo a boma ndipo anadandaula mchitidwe okuba zifuyo omwe anati wakula kwambiri m’boma la Chikwawa.

A Phiri apeza Chaleka kuti ndiolakwa ndipo analamula kuti akakhale kundende miyezi 30 komwe akagwire ukaidi wakalavula gaga.

Chaleka amachokera mmudzi wa Kachipepa m’dera lamfumu yaikulu Ngabu m’boma la Chikwawa.