A pulezidenti anakakamizidwa kukagwilira ntchitio ku nyumba yawo kamba ka njoka zomwe zinapezeka mu ofesi yawo mwadzidzi.

Mtsogoleri wa dziko la Liberia, George Weah

Malingana ndi malipoti, njokazi zomwe akuti zinali za mitundu yosiyanasiyana zinapezeka zikukwera khoma la office ya mtsogoleri wa dziko la Liberia, Goerge Weah – zinthu zomwe zinapangitsa achitetezo kuuza a Weah komanso anthu ena ogwira ntchito za boma mu ofesiyo kuti akapitilizire ntchito zawo ku nyumba ya mtsogoleriyu.

Njokazo zinathiridwa mankhwala a poizoni kuti zife.  

Lipoti la BBC lati ofesi ya pulezidenti wa dzikoli linakaikidwa ku ma ofesi a unduna wa zoona za kunja kamba koti nyumba yeniyeni ya mtsogoleri wa dzikoli linapsa ndi moto zaka zingapo zapitazo.

Nkhaniyi yachitika sabata latha lomweli ndipo a Weah amayembekezeka kubwelera mu ofesi yawo lachiwili, 23rd April.

Aka sikoyamba kumva kuti mtsogoleri wa dziko ku Africa achoke mu ofesi yake kamba ka nkhani ngati izi.

Mu chaka cha 2017, pulezidenti wa dziko la Nigeria, Muhammadu Buhari anakakamizidwa kukagwilira ntchito ku nyumba yawo kamba ka makoswe ambiri omwe anapeza mu ofesi yawo omwe anaononga zinthu zina ndi zina.

A Weah omwe analiso osewera mpila zaka zapitazo anasankhidwa ngati mtsogoleri wa dziko la Liberia mu chaka cha 2018.