Kadzidzi abweretsa mantha Kwa oyang’anira zisankho ndi apolisi m’boma la Ntcheu pa sukulu ya pulayimale yotchedwa Tchauya.
Sukuluyi ndi imodzi mwa malo amene zisankho zikuchitikira mu bomali.
Kadzidziyu yemwe anapezeka pa ma bokosi oponyeramo mapepala a zisankho anthu akavota akuti anakhala pamalopo usiku onse.
Ena mwa anthu omwe anali pamalopo anayesera kumuthamangitsa koma izi sizinaphule kanthu, ndipo anachoka mwakufuna kwake m’bandakucha.
Wachiwiri Kwa mtsogoleri wachipani cha Democratic Progressive Party (DPP) a Everton Chimulirenji analembetsera pa sukuluyi ndipo wavotera pomwepo. y