M’modzi mwa opikisana nawo pa mpando wa uphungu wa nyumba ya malamulo ku Blantyre City South a Moses Kunkuyu Avomereza Kugonja kwawo pa mpikisanowu.

A Kunkuyu omwe amayimira pa chipani cha Malawi Congress Party (MCP) Avomereza Kugonja kwawo kudzera patsamba la nkhani za mchezo la Facebook.

Mukulankhula kwawo a Kumkuyu afunira mafuno a bwino yemwe akutsogola pazisankhozi kudzera mumalipoti osavomerezeka a Noel Lipipa a chipani cha Democratic Progressive Party (DPP).

“Ndikufunira mafuno a bwino Noel Lipipa potsogola mu zisankho,” analemba Kunkuyu.

Anapitiliza popereka mdalitso kwa a Lipipa ponena kuti Mulungu awathandizire potumikira anthu a mudera la Blantyre City Constituency.

Akunkuyu anapitiliza pothokoza anthu onse amene anatenga nawo mbali popikisana pa mpando wa uphungu wa nyumba ya malamulo.

Mwa ena omwe amapikisana nawo ku kostichuwenseyi nd Osewera mpira wa miyendo ku timu ya Big bullets Fischer Kondowe, Oyimba nyimbo za chinyamata Penjani Kalua, Licy Kamwendo ndi Pemphero Mohande.