Mawu a wachiwiri wakale wamtsogoleri wadziko lino a Saulos Chilima okuti utsogole ndi osiyirana, apherezera.

Mawuwa apherezera pomwe a Chilima Asiyira a Everton Chimulirenji ofesi ya wachiwiri kwamtsogoleri wadziko lino.

Mumisonkhano yawo yokopa anthu a Chilima akhale akunena kuti ntchito ya utsogoleri si ya munthu mmodzi koma ndiyosiyirana.

Izi zachitika chomwechi kutsatira kulengeza kwa bungwe loona za chisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) kuti A Peter Mutharika ndi omwe apambana pa mpando wa mtsogoleri wadziko lino motsatiridwa ndi a Everton Chimulirenji ngati wachiwiri wawo.

Wamkulu wa pampando wabungwe loona za chisankho mdziko muno Justice Dr. Jane Ansah anafunira mafuno abwino a Mutharika ndi a Chimulirenji kutsatira kupambana kwawo pa zisankhozi.