Apolisi Ku Thyolo amanga m’zibambo wina wa zaka 54 yemwe dzina lake ndi Michael Chakwana kamba kopezeka akugonana kapena kuti akuchita zachisembwere ndi nkhumba.

Pa 03/7/19 nthawi ya 15:00 hrs Mr Fransis amasamba mu bafa kenako adasuzumira pa zenera la bafalo ndipo adawona mzibamboyo akugonana ndi nkhumbayo mu khola la ziwetozo.

Kenako Mr Fransis adapita Ku nyumba kwa bamboyo kukamufunsa chifukwa chimene bamboyo amachita n’chitidwewo koma bamboyo adawapepha a Mr Fransis kuti asawuze munthu wina aliyense za nkhaniyo.

Koma Mr Fransis adanena za nkhaniyo kwa achitetezo cha m’mudzi omwe adakanena za nkhaniyo kwa amfumu omwenso adakanena za nkhaniyo Ku polisi.

Bamboyo akuyembekezera kukawonekera Ku khothi kukayakha mlandu wopezeka akugonana ndi nkhumba.

Bambo Michael Chakwana amachokera m’mudzi mwa Mpiyama T/A Nchiramwera m’boma la Thyolo.