Bwalo la milandu Ku Rumphi lagamula kuti bambo wa zaka 53 yemwe dzina lake ndi Charles Phiri akakhale Ku ndende kwa zaka 14 kamba kopezeka wolakwa pa mlandu wogwililira msungwana wa zaka 14 yemwe ali kalasi ya Std 7 ndipo Bambo Charles Phiri ndi agogo ake a msungwanayo.

Pa 5 May 2019 mayi ake a msungwanayo ananyamuka ulendo wopita Ku Luzi komwe ndi kumudzi kwawo ndipo anasiya msungwanayo kunyumba kwawo ali pamodzi ndi azibale ake komanso ndi agogo ake omwe ndi bambo Charles Phiri.

Kunja kutada agogo ake a msungwanayo bambo Charles Phiri anamupepha msungwanayo kuti awapelekeze Ku nyumba kwawo, atafika Ku nyumba kwawo, agogo a msungwanayo anamuwuza msungwanayo kuti apite Ku chimbudzi cha panja chomwe chinali kuseli kwa nyumba, Kenako bamboyo anamulondola msungwanayo Ku chimbuziko kenako anamugwililira msungwanayo ndikumupatsa msungwanayo ndalama zokwana Mk 1000 kuti asawuze munthu aliyense za nkhaniyo.
.
Patadutsa miyezi iwiri anthu anayamba kuwona zizindikiro za chilendo pa nthupi la msungwanayo zomwe zidapangitsa kuti msungwanayo afunsidwe mafunso kenako msungwanayo anawulula kuti anagwililidwa ndi agogo ake bambo Charles Phiri.

Kenako msungwanayo adatengeredwa Ku chipatala cha Luzi komwe zinatsimikizika kuti msungwanayo ndi woyembekezera kapena kuti ali ndi mimba.

Nkhaniyi inatengeledwera Ku polisi kenako bambo Charles Phiri anamangidwa.
Bambo Charles Phiri anakawonekera Ku khothi komwe apezeka wolakwa pa mlandu wogwililira ndipo agamulidwa kukakhala Ku ndende kwa zaka 14.
.
Bambo Charles Phiri amachokera m’mudzi mwa Kamoza T/A Mkumbila m’boma la Nkhatabay.