Bungwe loona za madzi mchigawo chaku mpoto la Northern Region Water Board (NRWB) ladula madzi ku sukulu ya anthu osaona ya Ekwendeni School fo the Blind m’boma la Mzimba kamba ka ngongole yosachepera 1.5 milion kwacha yomwe sukuluyi ilinayo ku bungweli.

Frances Mkandawire yemwe ndi mphunzitsi wamkulu pa sukuluyi wati ngongoleyi yakhala koposera miyezi iwiri.

A Mkandawire anapitiliza kunena kuti vutoli lakhudza kwambili nkhani ya ukhondo pa sukuluyi.

Iwo anapitiliza kuti akulephera kulipira ngongoleyi kamba koti sukuluyi imayendera thandizo lomwe limalandira yomwe ndi 450, 000 kwacha pa mwezi, zomwe nkunena kwawo sizokwanira kuti ithetse mavuto omwe amakumana nawo.

“Kusowa kwa zipangizo ndiye vuto lomwe tikukumana nalo, ndalama yomwe timapatsiwa pa mwezi ndi 450, 000 kwacha yomwe siyokwanira kuti tigwiritse ntchito pa zofunikira za pasukuluyi, kuchokera pandalamayi timayenera tigule chakudya, zipangizo zokhudza ndi maphunziro, kulipira ngongele komaso malipiro a anthu ogwira ntchito zomwe sizinthu zophweka,” anatero a Mkandawire.

A Mkandawire anati akulu akulu a sukuluyi akhala akugundana mitu pofuna kuthetsa vutoli koma szikuthandiza.

Poyankhulapo ofalitsa nkhani ku bungwe loona za madzi mchigawochi a Edward Nyirenda anati kudula madzi ndiye inali njira yokhayo anali nayo poti zokambirana zinalephereka.

“Kukambirana ndi imodzi mwa njira zathu, tinayesera kukumana ndi akuluakulu a sukuluyi koma sizinapindule kanthu. Sukuluyi ili ndi magawo awiri tinadula gawo limodzi kuyembekezra kuti abwera poyera ndikulipira koma mmalo mwake anakumba mjigo zomwe ndikuphwanya chipangano,” anatero a Nyirenda.

Mmbuyomu unduna oona za maphunziro mdziko muno atafunsidwa zokhudzana ndi chithandizo cha anthu ofunika chithandizo chapadera mmasukulu, nneneri wa undunawu a Lindiwe Chide anati boma likugwirzana ndi anthu akufuna kwabwino kuti athandizepo m’malo ngati amenewa.