Dziko la Malawi likutaya 30 percent ya ndalama za ndondomeko yake ya zachuma chaka chilichonse kamba kamchitidwe wa katangale ndi ziphuphu zomwe akuti zikusokoneza ntchito zaboma.

Mgwirizano wa mabungwe omwe si a boma pankhani zolimbana ndikatangale, Alliance Against Corruption ndiwo wanena izi lolemba usiku pomwe mabungwe wa anakumana ndi ma komiti anyumba ya malamulo owona zachuma ndi malamulo.

Bungweli limafuna kukambirana ndi ma komitiwa njira zabwino zomwe makomitiwa zingatsate pofuna kuthetsa katangale mdziko muno.

Malingana ndi Action Against Corruption mgwirizano wa mabungwe omwe umafuna kuthetsa katangale mdziko muno lipoti la bungwe la united nations laonetsa kuti 30 percent  yandalama mndondomeko  ya zachuma ya mdziko lino zimasowa kudzera mukatangale chaka ndi chaka pomwe  6 biliyoni kwacha imabedwa ku khonsolo yokha.

Poyankula ndi ma komiti a zanyumba ya malamulo komanso azachuma akunyumba ya Malamulo, membala wamgwrizanowu a Moses Mkandawire anati makomitiwa ndiofunika pankhondo yolimbana ndi katangale.

A Mkandawire adzudzula boma polowelera muntchito zanthambi zina kamba koti izi zimasokoneza ndondomeko yoyendetsera nthambizi

“Katangale wapita patsogolo mdziko mwathu muno zizindikro siziri bwino. Chomwe timafuna ndichoti nyumba ya malamulo iziyesetsa kuthana ndi katangale kuti asapite patsogolo,” adatero  Mkandawire.

Poyankhulapo wapampando wa komiti owona za malumulo mnyumba ya malumulo a Kezi Msukwa wati ndiokonzeka kuthana ndi mavuto omwe mgwirizanowu wanena.

“Ndizabwino zomwe apanga anzathu amgwirizanowu,tikudziwa kuti pali Anti-Corruption Bureau (ACB) koma paokha zimathanso kuwapsinjanso,” adatero  Msukwa.

Mgwirizanowu unakhazikidwa pa 21October chaka chatha.