Wolemba Grecium Gama

Anthu okhala kwa mfumu yaikulu Nkhulambe boma la Phalombe adandaula ndi ndikukula kwa nkhalidwe katundu wamasiye pamene Bambo amwalira pabanja.

Izi zaziwika pamene bungwe la habitat for humanity linachitisa maphunziro omwe adaitainsa mafumu mankhasala komanso adindo osiyanasiyana omwe amawaphunzitsa kuipa kolanda katundu wamasiye.

Poyakhulapo mkulu oweruza milandu boma la phalombe yemwenso amaphunzitsa anthuwa a Damson Banda adati kulanda katundu wamasiye ndi mulandu zomwe adati anthu amene amachita nkhalidweli atapezeka olakwa antha kukakhala Ku ndende.

A banda adapepha anthu abomali kuti pamene alipabanja azilemba chikalata chosonyeza kagawidwe kachuma chawo mcholinga chopewa maphokoso omwe amadza munthu mmodzi akamwalira pabanja.

Agnes Mukoke mmodzi mwa anthu omwe akupindula ndi nyumba zomwe zikumangidwa ndi bungwe la habitation for humanity

“Ndupepha mafumu komanso adindo osiyanasiyana aziwalimbikisa anthu awo kuti pamene Ali pabanja azigawiratu Chuma chawo mkulemba mmapepala abwino bwino motsatira ndondomeko Zonse mcholinga chifuna kuchepesa mavutowa boma lino.

Poyakhulapo mkulu wa ntchito za habitat for humanity Stevie Makombe adati Iwo adaganiza zokomza maphunzirowo mcholinga chofuna kuwadziwitsa anthu omwe akuwamangira nyumba kuti asazalandidwe ndi anthu ena kutsogoloku.

” potengera ma lipoti omwe tidapeza kuchokera Ku khonsolo ya boma lino okhuza kulanda kwa Chuma chamasiye ndizomwe zidatipangitsa kuti tipereke maphunziro opidula anthu mcholinga chopewa nkhalidweli.

A Agnes Mukoke Ochokera mudzi kwa Mfumu yaikulu Nkhulambe adayamikira bungweli kaamba kaupangiri omwe alandira zomwe zithandizire kuteteza Chuma chawo komanso nyumba yomwe bungweli likuwamangira.

“maphunziro atithandiza kwambiri mudera lathu linokaamba koti poyamba sitimadziwa kuti munthu wamayi uli ndi ufulu woteteza Chuma chako pamene amuna ako amwalira . ndazindikira kuti kulemba makalata akagawindwe kachuma ndi ofunika zedi “,adatero a Mukoke