A polisi ku Lilongwe amanga Jonas Herbert wa zaka 37 kaamba komuganizira kuti wagwilira mwana yemwe ndi wa choir wa zaka 14.

Malingana ndi mneneli wa polisi ya Lingadzi a Cassim Manda ati mkuluyu ndi otsogolera choir ya pa mpingo wina.

Iwo ati gululi linali ndi ulendo sabata yathayi opita kwa Njewa komwe adapita kukachita maimbidwe.

Kumeneku akuti makosanawa adapatsidwa malo ogona, atsikana kwa okha komanso anyamata kwa okha.

Koma a Manda ati anthu adadabwa kuona mkuluyu akukakamila m’chipinda mudali atsikana-mo kufikira kutada.

Iwo ati usiku mkuluyu adapezerapo mwayi ogwiragwira msungwanayu mpaka kukwanitsa kugona naye.

Apapatu ndi pomwe m’mawa wake asungwanawa adakafotokozera makosanawa a pa mpingo omwe adakauza a polisi za nkhaniyi.

Mkuluyu akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu komwe akayankhe mlanduwu.

Herbert, amachokera ku Nathenje mfumu yaikulu Mazengera m’boma la Lilongwe.