Abambo anayi ali m’chitokosi cha polisi ya Lilongwe atapezeka akugulitsa Ngaka ya moyo ku Area 36 munzindawu.

Wachiwiri kwa mneneri wapolisi ya Lilongwe Khumbo Sanyiwa wati oganizilidwawa ndi a Stafford Omedi azaka 24, a Emmanuel Fabiano azaka azaka 30, a Paul Pelumbe azaka 41, a Bizwick Solomon azaka 40 komanso a Clement Juma wazaka 24.

Sanyiwa wati apolisi anakwanitsa kumanga abambowa atalandira uthenga kuchokera kwa anthu akufuna kwabwino kuti Omedi ndi Fabiano amagulitsa Ngaka yamoyo.

Ndipo apolisi anakwanitsa kumanga anthuwa pa malo ena omwesera mafuta pomwe anawapeza ndi nyamayi atayikutira musaka lomwe linayikidwa mu chikwama.

Sanyiwa wati awiriwa anatengeranso apolisi pamsika wa Kaphiri komwe anamanga anthu ena atatu omwe amayendesa nawo malondawa.

Oganizilidwawa akaonekera kubwalo la milandu posachedwapa kukayankha mlandu opezeka ndi Ngaka yamoyo opanda chilolezo.