Apolisi M`boma la Chikwawa akusungira mchitokosi mzimayi wa zaka makumi atatu ndi chimodzi (31) kamba kopezeka ndi fodya wamkulu wotchedwa Chamba.

Malinga ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Chikwawa Foster Benjamin, mzimayiyu yemwe dzina lake ndi Maria Mavuto ananjatidwa anthu akufuna kwabwino atatsina khutu a polisi m`bomalo.

Ma lipoti akuti pa tsikulo apolisi anamangaso anthu ena omwe adapezeka ndi mankhwala a mzipatala za boma mopanda chilolezo.

“Mayi Mavuto anamangidwa pamodzi ndi anthu ena anayi omwe anapezeka ndi mankhwala aku chipatala mopanda chiloleza,” anatero a Foster.

Mayiyu amachokera m`mudzi mwa Kalima Mdera la mfumu yaikulu Maseya ku Chikwawa ndipo akuyembekezeka kukaonekara ku bwalo la milandu posachedwapa.