Apolisi ku Blantyre akusungira mchitokosi m`zibambo wa zaka makumi atatu ndi chimodzi (31) yemwe amagulitsa kanyenya wa nyama pa msika wa zingwangwa chifukwa chobaya wa bizinesi mzake.

Mzibamboyu yemwe amatchedwa Mabvuto Kamkwecha Mwale anapalamula mulanduwu pa 23 Disembala chaka chomwechino.

kanyenya

Malinga ndi ofalitsa nkhani wa polisi ku Blanytre a Augustus Nkhwazi, pa tsikuli a Mwale anali limodzi ndi malemuwo omwe amatchedwa Saiwala Mwanduza (41) omwe amachitaso bizinesi yowotcha nyama pa msika wa zingwangwa.

“Koma ali mkati mocheza,panabuka kusamvana pakati pawo zomwe zinapangitsa a Mwale kutulutsa mpeni omwe adabaya nawo malemuwo pa mimba,” malingana ndi a Nkhwazi.

Posakhalitsa anthu anatengera malemuwo ku polisi ya chilobwe komwe anatumizidwaso ku chipatala chachikulu cha Queen Elizabeth Hospital koma tsoka ndi ilo adamwalira akungofika kumene.

Zotsatira za ku chipatala zidaonetsa kuti a Saiwala adamwalira kamba kotaya magazi ambiri.

Padakali pano, a Mwale ali mchitokosi kudikira kukaonekera pa bwalo la milandu komwe akayankhe mlandu okupha munthu.

A Mwale amachokera m`mudzi mwa Ndelemani mfumu yaikulu Kuntaja ku Blantyre pomwe malemuwo adali a m`mudzi mwa Mtambalika mfumu yaikulu Nkalo m`boma la Chiradzulu.