Patangotha miyezi ingapo chiletseleni mowa wotchipa wa midori omweso ena amati mkalabongo, Bungwe loona ndi kuyeza mulingo wa katundu la Malawi Bureau of Standards (MBS) latchotsa chiletso chake chomwe linayika pa mowawu kuti usapezekenso pa msika.

mowa wotchipa wa Midori

Mosakayikira ndi kuchotsera, achinyamata ku Malawi kuno atonyokaso mu 2018.

Bungwe la MBS lauza ma kampani omwe amapanga mowawu tsopano kuti ayambe kuika mowawu m`mabotolo a galasi osati m`mene amauyikira m`ma botolo a pulasitiki kalero.

Koma ngakhale izi zilichoncho, bungwe lina lomwe limaona za ufulu wa ogula katundu la Consumers Association of Malawi (CAMA), lati ganizoli silabwino pakuti muyezo wa zinthu zina zomwe zimaikidwa m`mowawu siunasinthe.

“Chomwe chasinthidwa m`mowawu ndi botolo chabe koma osati muyezo ndi mulingo wa zinthu zina zomwe zimaikidwa m`mowawu,” watero mkulu wa bungwe la CAMA, a John Kapito.

A Kapito apitiriza kuti izi zingopititsa patsogolo mchitidwe wa kumwa mowa mwa uchidakwa pakati pa achinyamata poti ndiwo amakonda mowawu chifukwa ndi wotchipa.

Chaka chatha, bungwe la MBS linalanda mowawu potsatira dandaulo lomwe anthu ndi mabungwe ena okhuzidwa anapereka za mowawu.