Mphunzitsi wamkulu pa sukulu ina ya primary ku Nkhotakota wadzipha kamba kopereka mimba kwa mwana wa sukulu.

Mphunzitsiyu dzina lake ndi Mr. Darwin Nkhoma ndipo adali mphunzitsi wa sukulu ya Kaweluwelu m’boma la Nkhotakota.

Mneneri wa polisi m’bomali  Ignatius Esau wati Mphunzitsiya adayamba kupanga zachisembwere ndi mtsikana wa zaka khumi ndi zinayi ndipo adamupatsa mimba. Pakadali pano mtsikanayi ali ndi mimba ya miyezi itatu.

Nkhaniyi itanveka m’mudzimo anthu ena anatsina khutu anthu amabungwe monga a “Girl Child education, ndipo pa 27, july mkulu wa chimasomasoyu adayendeledwa ndi amabungwe pa khomo pake kenako adamutengera pa sukulu yomwe amayang’anila. izi zidachititsa theng’enenge mkuluyi.

Ndipo atadziwa kuti mabungwewa akatsina khutu apolisii, Nkhoma adanamiza m’kaziwake kuti akukayan’ganila mbuzi ngati zidali zotsekeledwa koma Nkhoma sadabwereleso nyumba.

Patapita masiku awiri, Nkhoma yemwe amachokera m’mudzi mwa Kamphandika m’fumu yayikulu Kafuzila m’derali adapezeka atazikhweza chapafupi ndi nkhalango ya m’mudzimo.