Mtsogoleri wa Chipani chotsutsa cha United Democratic Front (UDF), Atupele Muluzi wati iye ali ndi kuthekera konse kotukula dziko la Malawi.

Muluzi in the middle

Muluzi wayankhula izi lachitatu lapitali pa msonkhano waukulu omwe chipani chake chidapangaitsa ku Blantyre pokonzekera zisankho zomwe zili nkudzazi.

“Ndimakonda dziko la Malawi ndipo ndili ndi masomphenya osintha zinthu. Ndimakhulupilira kuti kusintha ndikotheka pokha pokha ife ayini ake titaikirapo chidwi,” atero a Muluzi.

A Muluzi anonjezera kunena kuti ulimi wa fodya siukubweresaso phindu lokwanira choncho dziko la Malawi langoyenera kupeza njira zina zobweretsera chuma.

Ena omwe anayankhula ku msonkhanowo ndi mtsogoleri wakale wa dziko lino Dr Bakili Muluzi omwe anati nthawi yatha tsopano kuti atsogoleri azipani azilimbana ndi ndale zokokanakokana.

Iwo anapereka chitsaonzo cha mkazi wa mtsogoleri wakale wadziko lino, Callista Mutharika omwe mbuyomu m’mawu awo adanena anthu ena ochita ndale kuti ndi matchona ati kamba koti adakhalitsa kwambiri m’maiko akutali.