Banja la a Buleya Lure omwe adaphedwa ali m’manja mwa apolisi pa nkhani yokhuza kusowa kwa m’nyamata wa chi alubino wa zaka 14 Ku Dedza likufuna ndalama zokwana Mk 250 miliyoni ngati chipepeso kuchokera Ku boma.

Yemwe akuyimira banjalo pa mlanduwu a George Divason anena kuti banja la a Buleya Lure likufunanso kuti apolisi omwe akukhuzidwa ndi imfa ya malemu Buleya Lure azengedwe milandu pasanathe sabata imodzi kuyambira loweruka lapitali ndipo awopseza kuti izi zikakanika kuchitika iwowo ayitengera nkhaniyi Ku bwalo la milandu.

Ripoti la bungwe la Malawi Human Rights Commission lidanena kuti apolisi okwana 10 akukhuzidwa ndi imfa ya a Buleya Lure, Iwo adafa atamenyedwa komanso atatenthedwa ndi nyetsi za magetsi pa nthawi yomwe iwowo adali nchitokosi cha apolisi. Malemuwa adaphedwa pa 20 February 2019 m’manja mwa apolisi Ku Lilongwe