Ogwira ntchito ku nyumba yachisoni (Mortuary) yemwe wakhala akugwira ntchito yake kwa zaka zopitilira (32) wanena kuti amasangalatsidwa ndi kugwira ntchito ndi anthu akufa chifukwa ndi odekha.
Mzibamboyu yemwe amagwira ntchito ku nyumba yachisoni ina mu dziko la Uganda walongosola ubwino komanso mavuto omwe amakumana nawo pa ntchito yake.
“Nthawi yomwe ndimkamwa mowa, pamapezeka anthu ena omwe amakana kumwera nane chipanda chimodzi ati poti ndine ogwira ntchito ku motchare. Anthu ena amachita kukana ndi kundipatsa moni wa pa dzanja yemwe,” a Basil Enatu anawuza DailyMonitor.
Koma ngakhale pali zovutazi, bambo Enatu ananena kuti ntchito yawo amaikonda chifukwa paliso ubwino wina omwe amauona.
“Ndimakonda kugwira ntchito ndi mitembo chifukwa simadandaula kanthu, simapanga za chipolowe, komanso ndi yodekha kwambiri. Tonse tikudziwa kuti kaya ndiwe olemera kaya osauka koma tsiku lina udzafa ndipo tizakakwililidwa mofanana kumanda.”