Mzibambo wina wachikulire mu dziko la Zambia wamangidwa kamba kokupha mkazi wake pomubaya ndi mpeni achibale ndi anthu ena akuona.
Malingana ndi malipoti, izi zachitika pamene awiriwa anakangana kamba ka nkhani za m’banja m’mudzi wa BundaBunda m’boma la Chongwe, lachiwiri sabata yatha.
Mzim’bambo wazaka 79 yu akuti adabaya mkazi wake, Iness Shumba (65) kopitilira ma ulendo asanu kunyumba ya mchemwali wa mkazi wake komwe obaidwayo anapita kukatula nkhani ya nkhaza za m’banja zomwe amaziona kuchoka kwa mamuna wakeyo.
Wachiwiri wa Mneneri wa apolisi m’boma la Chongwe mu dzikoli, Danny Mwale adatsimikiza za nkhaniyi pomwe amayankhula ndi atola nkhani mu dzikoli.
A Mwale ndi apolisi anzawo omwe anathamangira komwe izi zinachitika ati obaidwawo anali akupita kunyumba ya amfumu kukaaneneza mamunayo pa mlandu wa nkhanza za m’banja.
Padakali pano, m’bambo wachikulireyu akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu kukayankha mulandu okupha.