Patapita masiku ochepa boma la South Korea litakana diso liri tuzu dzuwa liri pa liwombo kuti iwo sanagwirizane ndi dziko la Malawi pankhani yotumiza athu kumeneko kuti azikagwira ntchito, nawonso aja amati apita ku Kuwait adzinyenga ndichala boma litawabweza kuti asapite kaye.

M’malo mwake, iwo apemphedwa kudikira sabata ziwiri kapena kuposera apo kuti boma libawunika zina ndi zina.

Zatsala za ku Dubai timva ngati ulendo ulipo. Tiyeni a Malawi tingoyamba kulimbikira kunkuno basi mukachoka inu adzawavotera ndani Amai.