Bwalo lalikulu la milandu kapena kuti High Court ku Lilongwe lalamula kuti a Lester Maganga omwe akuwaganizila kuti anapha a Allan Witika akhalebe ku ndende kufikira a Police amalize kafukufuku wawo pa nkhaniyi.

Chigamulochi chikubwera kamba kakuti masiku apitawa a Maganga anapempha belo. Oweruza milandu Justice Mzondi Mvula wati a Maganga anafulumila kupempha belo masiku omwe a Police anapempha kuti iwo akhalebe akusungidwa kundende asanathe. Pamene a Maganga anakaonekera ku bwalo la magistrate masiku apitawa,apolisi anapempha kuti a Maganga akhalebe akusungidwa kwa masiku 90 kuti atsirize kufufuza kwao.

A Mvula ati malingana ndi malamulo adziko lino, a Maganga amayenera kupempha belo masiku 90 akatha.

Justice Mvula wati kwatsala masiku 68 kuti a Police amalize kupeza umboni womwe akufuna pa nkhaniyi.

Padakali pano, bwaloli lalamula kuti a Police adzakhale atamaliza kafukufuku wawo pofika pa 23 January, ndipo atsindika kufunika koti mulandu umenewu usadzachedwe bwaloli likadzayamba kuzenga nkhaniyi.

A Willie Zingani, yemwe ndi malume amalemu Allan Witika, ati chomwe akufuna ndi chilungamo

Innocent Kubwalo yemwe akuimira a Maganga, anati sangayankhule zambiri kufikira atamva amaganizo a Maganga pa chigamulo chomwe bwalo lapereka.

Source: MBC Online